Achinyamata ku Mangochi apempha Boma kuti lichilimike pothandizira ndi ngongole achinyamata amene Ali ndi luso losiyanasiyana la manja.

Pa 15 July chaka chilichonse dziko lapansi limakumbukira luso la ntchito za manja la achinyamata.

Mutu wachaka chino ndi Kuwonetsa luso la achinyamata kuti anthu antchito za malonda awagwilitse ntchito “Unvailing youths skills which investors can target”

Achinyamatawa adandawulira Boma kuti silikuchita kanthu powonetsetsa kuti ngongole za NEEF zikufiikira achinyamata ochuluka omwe Ali ndi maluso.

Iwo ati ngongole za NEEF, pamwamba poti zimachedwa, zimavutanso kuti zipezeke.

Poyamikira lingaliro lopeleka ntchito kwa anthu okwana 1 million omwe ndi achinyamata, ma bungwe osiyanasiyana ku Mangochi adandawura ponena kuti Boma silikuyika chidwi pofuna kutukula ntchito za achinyamata kuti ntchito 1 million zipezeke.

Pa mwambowu, akulu omwe anapezekako ndi monga Bwana nkubwa wa Boma la Mangochi Raphael Pilingu, Phungu wa Pakati pa Boma la Mangochi Victoria Kingston, Senior Chief Chowe, District Youth Officer Kumbukani Manda komanso Zakiliya Allisah wapampando wa mabungwe achinyamata m’bomalo.